Templates by BIGtheme NET

Airtel Top 8 yawilira pamene anayi afika mu ndime ina

Your ads will be inserted here by

Easy Plugin for AdSense.

Please go to the plugin admin page to
Paste your ad code OR
Suppress this ad slot.

Ofooka akugwa ndipo olimba akudutsa mu Airtel Top 8 pamene anayi alongeza.

Zinthu zafika pa mponda chimera mu mpikisano wa Airtel Top 8 pamene matimu anaya alongeza ndipo anayi ena awolokera mu ndime ina.

Zitha kukhala kuti kubwera kwake kudachititsa mpungwempungwe pa nkhani za masewero dziko muno koma tsopano mpikisano wu wadza ndi mkokomo kutsatira kutha kwa ndime yake yoyamba.

Matimu a Blue Eagles, Mafco FC ndi Azam Tigers anawonetsedwa nsana wa njira dzulo pa 20 May 2017 ndipo timu ya Nyasa Big Bullets yasamutsidwanso mu mpikisano lero ku Mulanje.

Mmene zateremu ndiye kuti matimu a Be Forward Wanderers, Moyale Barracks, Kamuzu Barracks ndi Silver Strikers zawayendera ndipo akhala akuthambitsanabe.

Malinga ndi mayere omwe achitika ku Mulanje, Be Forward Wanderers yodzika bwino kuti Nyerere igubuduzana ndi Moyale Barracks ya mu mzinda wa Mzuzu ndipo Kamuzu Barracks itengetsana chulu chachula ndi anzawo a mu mzinda wa Lilongwe Silver Strikers.

Masiku a masewero a mu ndime imeneyi akhale akulengezedwa pamene anthu akhale akudikira mwa chidwi kuti aziwonere amene atenge chikho chimenechi mu chaka chake choyamba.

Facebook Comments

About MalawiNewsHub Reporter

One comment

  1. I’m not that much of a internet reader to be honest but your sites really nice, keep it up! I’ll go ahead and bookmark your site to come back later on. Many thanks